Mlakatuli Charlie David Bandah

Easy comes easy goes ๐Ÿ’ช

26/10/2023

Fourth anniversary ๐Ÿ™ˆ๐Ÿ™ˆ๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚

With my simcard I mean ๐Ÿคฃ๐Ÿคฃ

01/09/2023

Zilumika zikati zithamange.

Mpadzana paja china chilumika tidakwangula
Tili kachinja m'dzikhatho zamama olema ndi uchembezi
Simudakhumbile zonditayila nchigwembe
Koma pondifungata ine m'dzikhatho zanu mnyengo yonse
Kukoma mtima kwanu kwandionesa dziko
Lodzala ndi mayenje pena mayiwe aumphawi
Koma chikondi chanu Mama chidali chonona
HAPPY BIRTHDAY TO ME

09/08/2023

ZWELIWE....... Wanna be the latest poem full of maturity and everything about life is in there.

ZWELIWE ๐Ÿ˜ฅ๐Ÿ˜ฅ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ

25/07/2023

Happy birthdaySylvester Kalizang'oma UNKALINDANJI MOYO๐Ÿ˜ฅ๐Ÿ˜ฅ๐Ÿ˜ฅ๐Ÿ˜๐Ÿ˜๐Ÿ˜I believe one-day I'll be like you Mr

05/07/2023

Pipo hawร yu there๐Ÿ™Œ

22/05/2023

Tell others to follow my page please ๐Ÿšถ๐Ÿšถ๐Ÿšถ๐Ÿšถ

16/05/2023

MISOZI YOSAKATA

Nkale lija Mayi //
Chinangwa tidabzala //
Pondisiya ndili kachinja zitsakano ndisadaphukile //
Pomuthotholetsa nchimwali wanga bele alinchikuta๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ
Asadakhambe //
Masomphenya mutatipalira //
Potifungula maso ndi mapilikilanilo //
Lerolino zilumika zingapo
Kuchitseko zathera๐Ÿšถ๐Ÿšถ
Mutaumitsa mtima potileka ife //
Malo omwe timakhala,chisimba chomwe timagona //
Nchomwe chija mudatisiyila makedzana //
Mwina mukadakhalako,,
Lowala tsogolo tikadakhala nalo //
M'masaya mwanga //
Misozi ndiyo itsikila , misozi yosakata๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ
Kumbuto yakunsabwera ndiko ubwenzi mudapalana nako
Mayiwanga mzimu wanu uwuse mumtendere๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ

28/04/2023

KACHEPA KAYENDA KAKAFA KAKHUMBA MTENGEDZO๐Ÿ˜ฉ

15/04/2023

Kachilembo aka X

Nkododometsa kozingwitsa
Enatu komweka amada nako kukhosi akakakumbukila
Misozi yosakata imathamangitsana mwaliwilo yandawala
Maka akaganiza kuti adataya bomwetamweta
Komweka phwete losaneneka kamawakodolera chikumbu mtima chikawafungata bongo.

X

Kagwilitsidwe kake ntchito noosiyanasiyana
Kotengera maphunzilo ako
Pena kamagwila ngat C
Ozitsa nkumati Z
Ndithudi X kachilembo kopweteketsa moyo
๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ๐Ÿ˜ญ

05/03/2023

Good morning people.

Maluzi asakuluzisen
Auzen kuti simuwagonjera
Tsiku lina azakuthawani mutakwera njare๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚ hustle ever๐Ÿ’ช๐Ÿ’ช

14/02/2023

NDIWE MY VALENTINE

Kanyama kanga kamiyendo iwili yopilingidzana
Kathupi logwilika mousa mudyo
Kowala konga nthanda yakumawa
Ake maso akati phethi
Kakodola chipemba chamtima wanga
Timawu tanthetemya akandibzyikulira
Kadodometsa anga maganizo

Sulira zambiri Dona
Liwu lokhali loti ndimakukonda
Limapeza mbuto m'mapilikanilo nwako maka ngati mgaiwa ndi denje lokupa ndi chidulo chamtengo wanjale palilime lako ladutsa

09/02/2023

Sylvester Kalizang'oma the great man in poetry. NAYI NKHATA YAMALIRO & UNKALINDANJI MOYO ESHIII!!.

23/01/2023

Ndikukhumbile kufika pamthobo pa ulakatuli olura monga momwe adachitila Silvester Kalizang'oma he is my favorite

17/01/2023

Ndinali nditsiku lopambana kwambiri lamulungu pokumana maso ndi maso ndi Mlakatuli Silvester Kalizang'oma, Mchochombe Hardson chamasowa ndi ena ambili. May Allah bless me and give me more energy and desire to reach my destiny.๐Ÿ™

10/01/2023

IN THE WILDERNESS

The step we move
With long strides we walk
Bare footed
In thorny bushes towards the green pasture

03/01/2023

Tsogolowe............. Out now

26/12/2022

Ntchito tugwilatu

19/12/2022

Motivational speaker once said

I was studying using my father's cigarette stabs look now I am a pilot ๐Ÿคฃ๐Ÿคฃ

08/12/2022

Morning people

03/12/2022

Let's thank God for everything we have life itself it's a good thing ๐Ÿ™

02/12/2022

Mayeso atuluka
Ankayembekezera ma teen
Ankatinyaditsa polankhula mwansulizo
Ati sukulu amaliza ali ka teen
Lerolino kuli chuu
Agwa nawo mayeso mwaphokoso
Anga chopanda kanthu chitini

๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚๐Ÿ˜‚

30/11/2022

CHIKATI CHITHAMANGE CHILUMIKA

Shaaa! Mpadzana paja tidakondwera,
Inde khisimisi
Tikadali achisodzera
Tinkaonatu kuchedwa ife
Maka makolo potifunkhila nkutigulira kabudula ndi malaya?
Mtimatu siunkakhala m'malo
Poona masiku kuchedwa
Chilundu cha amayi
Chitamanga mfundo pazovala zanga

Zilumika nkumapita
Nsinkhu nkumakula
Lerolino kukhosi kwada
Pozindikila kuti kuchitseko nawo masiku akuthera
Jontchololo zanga ndevu
Zidzetsa chitonzo
Indee nyontcholi opanda ngakhale lobola

Nawo azichemwali
Akhumbila kudzalawa kaja kadaunda madzi pagome landekha
Kwinaku namagetsi wanga akusonkha moto wondikupila phala lantombera

Koma lerolino ngakhale chola
Chachikumba chambuzi nkapenya
Mununkhila umbeta wodzala ndimaluzi omangila zisakasa zauumphawi

Koma nazo zaka zikati zithamange
Zopezetsa makolo nkhani
Yofuna kukusamutsa
Pakuti chingwa pagome lawo subweretsa
Zilumika zili mwandawala
Zikufuna kutikankhila kudzenje lamazunzo amawanja osokonekera

๐Ÿคฃ๐Ÿคฃ๐ŸคฃZaka zikuthamanga๐Ÿƒ๐Ÿƒ๐Ÿƒ๐Ÿƒ
Yolembedwa ndi Mlakatuli Charlie David Bandah.

25/11/2022

Direction is more important than speed

18/11/2022

Kuyambilanso etii okay fine. Palibe kufooka mpaka chili mwaine chitatumphuka
Nkufikila ena

17/11/2022

Hack this again

17/11/2022

Mwandionera chiyani koma??

Mpaka tsamba langa la ndakatulo kundisokonezera?
Mukadandiuza nkadakuthangatani
Koma shaa
Kufuna kwanudi kuchitike

Want your public figure to be the top-listed Public Figure in Blantyre?
Click here to claim your Sponsored Listing.

Category

Telephone

Website

Address

Blantyre
Other Authors in Blantyre (show all)
World of creativity writings World of creativity writings
Blantyre

I believe to entertain people while motivating them

Sid Short Stories Malawi Sid Short Stories Malawi
Blantyre

Stories and Poems

Mindful life thoughts Mindful life thoughts
Blantyre

Let's grow together with a delicate balanced mind

Ajida Osman Ajida Osman
P. O. Box 30644 Blantyre 3
Blantyre

Geoffrey Maulidi Geoffrey Maulidi
P. O. Box 31256
Blantyre

Geoffrey Maulidi, popularly known as Ndimakhala Busy, is a writer among other things. He studied Pol

PREDO PREDO
Blantyre

Highly Favored

Priscilla Phiri Priscilla Phiri
Chapima
Blantyre

A Scilla is a person with a role either to promote, display or advertise commercial products (notably fashion clothing in fashion shows) or to serve as a visual aid for people who ...

Lawrence Kadzitche Lawrence Kadzitche
Off Makata Road
Blantyre

fiction writer

Alinafe Alinafe
Blantyre

Robertoh 001 the poet Robertoh 001 the poet
Blantyre

Providing unfolded beauty of poetry