Stellah's short stories

Stellah's short stories

You may also like

Thola imali esheshayo
Thola imali esheshayo

this page is for only entertainment

07/05/2022

Funny ppl

02/05/2022

🔥✔

29/09/2021

*_Grand P* { *Moussa Sandiana Kaba}*
_
_Star Warelo_ ✍️

Lero tiyeni tiwerenge History ya m'modzi mwa anthu odziwika muno mu Africa--- maka maka ku west Africa ndikunenatu za _Grand P ._

✍️_Grand P_ ili ndi dzina lomwe amadziwika nalo lodyela, koma iye dzina lake lobadwa nalo ndi { *Moussa Sandiana Kaba}* Grand P anabadwa pa 13 October 1993-- adabadwila ku dera lomwe limatchedwa Sanguiana Nabaya mu dziko la kwawo ku Guinea (pa chaka cha kubadwa apo ena amati ndi 1990 koma mukufufuza kwa ine ndapeza malo ambiri palembedwa 1993) , *Grand P* pakanali pano amapatsidwa ulemu mu Africa ngati m'sangalatsi kamba ka nyimbo zake zosangalatsa . *Grand P* atabadwa ma dokotala adadzamupeza ndi matenda pa chingelezo matenda awa amatchedwa ( progeria) matenda awa amapangitsa k*ti munthu thupi lake lizioneka okalamba ngakhale ali mwana, komaso thupi limakula lonyentchela & mau amaveka ngati kamwana. Grand P ali wa chichepele ati palipose pomwe an'kayenda amakhala akusekedwa ndi ana azizake ngakhaleso anthu akulu akulu, koma iye sadafooketsedwe ndi kusekedwa komwe ena an'kamuseka. *Grand P* luso lake loyimba lidaonekela atatulutsa ka video clip komwe adayimba nyimbo yofunila mafuno abwino team yokankha chikopa { *_Guinea Football National Team}_* ndipo Africa Cup of Nations yomwe idapangidwa host ndi dziko la Egypt mu chaka cha 2019 Grand P adaitanidwa kumeneku kukasangalatsa anthu , Grand P wakhala akunena monenetsa k*ti sadzatengela style kapena k*ti mayimbidwe a wina aliyese iye adzafa ndi mayimbidwe ake ake. Grand P poyankhapo za anthu omwe amamuseka maonekedwe ake wakhala akuyankha poyela k*ti (poti Mulungu adamulenga choncho--- icho ndi chifunilo cha Mulungu-- komanso kamba ka matenda omwe adabadwa nawo palibe chomwe iye angapange) Grand P amapitiliza kunena k*ti akudziwa zoti pali anthu omwe amamukonda ngakhale maonekedwe ake ali onyentchela, and adati amadziwa zoti pali anthu ena amaseka maonekedwe ake omwe iye sadachite kufuna amamaliza ndi mau oti { _such is life you can please everbody}_ --- ali wa m'ng'ono Grand p ak*ti san'kadziwa m'komwe k*ti tsiku lina adzakwela ndege koma pakanali pano iye ndege amakwela momwe wafunila, atangoyamba kufuna kukhala oyimba Grand P adathandizidwapo ndi anthu omwe amasangalala ndi nyimbo zake ena mwa iwo m'kukhala anthu a ndale monga a *Baidy Aribot* akulu awa ndi Vice governor of central Bank of Guinea ndi omwe adapanga dongosolo loti Grand P akwele ndege ulendo okasapota team ya m'pila wa mwendo ya dziko la Guinea ku African Cup Finals omwe udachitikila ku Egypt--- atachoka ku Egypt adaitanitsidwa ku Mali komwe adakakumana ndi anthu omwe ali ndi matenda ofanana ndi omwe Grand P adabadwa nawo, izi zidapangitsa k*ti ambiri anthu ku dera loyandikana ndi dziko la Guinea ayambe ku mukonda Grand P-- olemba news paper adadzamutcha Grand P k*ti ndi New ambassador of the good dedicated .

_Star Warelo --_ ✍️

Pa ulendo wake omwe adali ku Mali Grand P adapemphedwapo kuimba ndi oyimba otchuka wa ku Mali *(Oumou Sangare--- Sidiki Diabate)* komaso adaitanidwapo ndi kukakumana ndi Saidou Keita mwana wa president --- Grand P sadasiile pompo adakafikaso ku Ivory coast komwe adakaimba ndi DJ Arafat , El Poueblo Bravador ndi ena ambiri oyimba odziwika ku Ivory coast, momwe an'kayenda mu maiko onsewa amayenda namakumanaso ndi anthu omwe adabadwa ndi nthenda yofanana ndi yomwe iye Grand P adabadwa nayo monga Ambassador for short people. Grand P kumbali ya chikondi ali pa ubwezi ndi m'tsikana wa ku Ivory coast dzina lake *Eudoxie* m'tsikana uyu amadziwika ndi dzina lodzichemelela loti Kim Kardashian of Africa , ku maiko a ku West Africa Eudoxie amawelengedwa k*ti ndi yemwe ali ndi matako *(mbina kapena k*ti chinyophilo)* kuposa akazi ose a ku west Africa, Grand P adafusila Eudoxie mu August 2020 ndipo adati pali chiyembekezo choti adzamangitsa banja lawo mu 2021, koma ambiri anthu akhala akunena k*ti Eudoxie adavomela Grand P pongofuna ndalama osati chikondi koma m'tsikanayu wakhala ak*tsutsa izi k*ti ndi sanje chabe za anthu. Pa live show yomwe idakozedwa ndi a Kerfalla Kante mu 2019 ku Conakry peoples place a Grand P adakaikilidwa ndi anthu ambiri zoti angakwanitse kuimba pa Stage komatu Grand p adaimba pa show iyi posalingalila za matenda kapena maonekedwe ake, osaiwala monga ndafotokoza pamwambapo k*ti adali m'modzi mwa ma delegates omwe adapita ku Egypt ndi team ya Guinea ku Africa Cup of Nations izi zidapangitsa kwambiri k*ti Grand P ayambe kukondedwa ndi anthu ambiri mu Africa ndi maiko a ku Ulaya--- monga ndafotokozapo pamwambapo k*ti Grand P waimbapo ndi oyimba odziwika ku Guinea adaimbaposo ndi Azaya, King Alasko ma collaborations oterewa adapititsa mbiri ya Grand P patali--- Grand P ali ndi Album yotchedwa (title) I *Khadi nanna"* ndi ma single angapo monga " *Grand P Barana" Life" Syli"* mu 2019 adapangidwa feature ndi Sidiki Diabate single " *Irhafama* " pa 11 September 2020 adapangidwa feature ndi Boncena mu single title " *Amour Ndoto* ".

*_Star Warelo*_

Grand P ndi m'modzi mwa oyimba olemela (rich) ku Guinea pali chiyembekezo choti ali ndi ndalama zosachepela $10 million US dollar, Grand P eya ndi oyimba komasotu amapanga nawo za ndale (politics) Grand P adalengeza k*ti apikisana nawo pa zisankho zomwe zidachitika mu dziko la Guinea mu 2020 mwezi wa October zisankho izi adawina ndi a { *Alpha Conde}* term ya number 3 koma ambiri adati a Alpha Conde adabela zisankho izi # tiyeni tikumbukile k*ti a Alpha Conde adalandidwa boma ndi asilikali masabata angapo adutsawa. A Grand P popanga ubwezi ndi m'tsikana wa ku Ivory coast (Eudoxie Yao) zidawapangitsa kukhalaso ndi fun base yaikulu mu dziko la Ivory coast. Pa kufuna kupikisana nawo kwa bwezi lake Eudoxie adati amuna ake omwe ndi president wa m'tsogolo muno wa dziko la Guinea, adafuna k*ti naye ayimile u president pa zisankho za mu Ivory coast ndi thandizo la ndalama zopatsidwa ndi bwezi lake Grand P zitamuvuta iye adati ngakhale zamuvuta ku Ivory coast iye Eudoxie ali ndi chikhulupilo choti one day adzatchedwa first lady wa dziko la Guinea

✍️
Ndimalize motere *(Grand P)* ndi nick name-- kapena k*ti dzina lodyela 👏-- dzina lobadwa nalo ndi { *Moussa Sandiana Kaba}*

✍️Kwawo ndi ku { *Guinea* } --- Fiance kapena k*ti bwezi lake ndi *(Eudoxie Yao)* wa ku Ivory coast.

✍️ Mu 2020 adasaina contract ndi ma company a ku America awiri omwe amamupanga sponser.

✍️ Za family yake komanso momwe adakulila ku ubwana ndi maphuzilo ake sindidathe kupeza information yotereyi.

✍️(Progeria) awa ndi matenda omwe *Grand P* adabadwa nawo, matenda awa munthu amayamba kukalamba maonekedwe ali wang'ono, munthu amatalika kufika pa 1 meter osadutsa, pa scale amakwela 25 kilograms osadutsa.

✍️ mu 2020 *Grand P* adali olemela $10 million US dollar, pali chiyembekezo choti pofika mu 2021 ali ndalama zodutsa $12 million US dollar--- Grand P ali ndi nyumba ya pamwamba kwambiri ( mansion) ili mu m'zinda wa (Conakly) ku Guinea ndipo ndi m'modzi mwa oyimba ( musicians) olemela muno mu Africa 👏 Grand P ali ndi ma galimoto a pamwamba monga Lamborghini, Masserati ndi zina zotelo.

✍️ *Grand P* ndi member wa chipani chotchedwa (ACU) ndipo ali ndi chikhulupilo k*ti adzawina ma primaries ndi kuimila chipanichi pa zisankho za 2025.

Ndateremu ine ndakwangula kufotokoza mbiri ya Grand P monga mwa pempho lanu ma Star

👏 Mu comment box nenani k*ti next or Dzimele

; Nkhaniyi yachita kumatulidwa kuchokela ku group lathu lolipilisa la Star Walero family, ndi K300/R15 pamwezi, mukationa zii pano tikumakhala kumeneku and nkhan zambiri zikumavumbulukaso kumeneko. Tipezen ku inbox or pa Whatsapp
+265 99 000 22 70, +265 881 40 30 10 & +27 71 099 2089 k*ti mujoine lero!

@ *Dzufunadzimelendevuidzidzi*

Timeline photos 06/09/2021

ADAMS WATISIYA ATAKOMOKA KWA ZAKA 39

Bungwe loyendetsa masewero a mpira wamiyendo m'dziko la France lalengeza k*ti katswiri wawo, Jean-Pierre Adams yemwe anakomoka zaka 39 zapitazo wamwalira lero chakum'mawaku kuchipatala chotchedwa Nimes University Hospital.

Jean-Pierre Adams, yemwe anabadwira mumzinda wa Dakar m'dziko la Senegal, anakomoka mwezi wa March m'chaka cha 1982 madotolo atalakwitsa magwiridwe a ntchito awo pamene amamupanga opaleshoni ya pa bondo.

Katswiriyu, yemwe wasewelerapo timu ya France m'masewero opitilira makumi awiri, wamwalira ali ndi zaka 73 ndipo wasewelerapo matimu monga Nimes, PSG komanso Nice.

Chikomokeleni osewerayu, France yatengapo zikho ziwiri zampikisano wa padziko lonse pachingerezi World Cup; koyamba mu 1998 kenako mu 2018.

20/08/2021

*DID YOU KNOW*...?..
1. Pa anthu 100 alionse, ndi anthu awiri okha mungawapeze ndi maso a green.
2. Agalu nthawi zina amalenga ngat adwala cholinga kungofuna attention ya amene amayang'anila
3. Mphevu nkachinyama komwe kamanyasidwa kwambiri munthu ukakagwira, kungokagwra or kukagunda kamathamanga pompopompo kukazisuka thupi lonse...
Star Walero family ..
4. Ku England kuli mtsikana kamwana kenakake kotchedwa Olivia Farnsworth, iyeyi anabadwa ndi ma chromosome odabwisa kwambiri nthupi mwake (Chromosome 6 Deletion) samva njara, samva kupweteka and satopa k*ti akufuna kugona. Mu 2016 anagundidwa ndi galimoto kwambiri anthu kuona choncho koma sanavulale kwambiri and sanamveso kupweteka, ndipo ma doctor anampasa nickname ya "Bionic girl"..Amachit kufuna ekha k*ti adye not k*ti wamva njala, and kugona not k*t watopa.

5. Mtima wa Blue whale (chinsomba chachikulu umalemela 600Kg)
6. Mtundu weniweni wa dzuwa si Yellow koma white.
7. Ku Norway kuli church dzinalake Stave Church, chinamangidwa zaka 800 zapitazo opanda nsomali, mitengo basi koma sichinagwepo and ncholimbabe pano.



8. Jamaica flag ndi flag yokhayo padziko lapansi imene ilibe mtundu wa red, blue or white pa mbendela yake.
9. Basenji ndi galu yekhayo amene samatha kuhuwa, sahuwa ngat agaluwa enawa akafuna kuluma amangoluma mwa silent and akamathamangisa munthu sahuwa ndati.
10. Munthu kungopezeka wapha Njovu ku Sri Lanka umaphedwa siku lomwelo..
```KODI MUKUDZIWA??```
Ma facts onsewa akubwera chifukwa cha group yathu yolipilisa ya Star Walero family, ndkumene kumavumbuluka nkhani zambiri and zambiri zimayamba kuponyedwa kumeneko zisanafike pano..Ndi K300/R15 pamwezi. Tipezeni pa; +265 99 000 22 70, +265 881 40 30 10 and +27 71 099 2089 k*ti mulowe ku family...
Phosomthumba sanatope ndikupitilizabe👇🏽👇🏽👇🏽..
11. Plover bird ndi mbalame yokhayo imene imatha kukhala mkamwa mwa ng'ona koma osadyedwa. Chinsinsi chake ndichak*t imachosa nyama yokanilira mmano mwang'ona iyo kumadya, ndipo ng'ona imakondwela

12. Australian Bussinessman komanso Blue Star line company, Clive Parmer, Wati akupangaso Titanic ship ndipo iyi ikhala Titanic 2.0. Palmer analengeza izi mu 2018 k*t by 2022 stimayi izakhala itayamba kuyenda, Titanic 2.0 ati ikhala yayikulu and yabwnoso kwambiri ngati yoyamba ija ndipo izinyamula anthu 2435, ndalama zomwe zalowa kupangla sitimayi ndi $500M

13. Ku Australia kuliso mzinda omwe uli pansi padziko otchedwa "cobber pady".. Mu 1915 kumkatentha kwambiri ku Australia mpaka temperature ya 50 degrees ndipo anthu anayamba kuganiza k*t bwanj titamakumba pansipa tizikhala ndipamene anayamba kupanga, mpaka pano ndi City yomwe ili pansi pomwe timapondapa. Kuli Manyumba, church, misika ndi ma hotel.
14. Indonesia ndi dziko limene kuli anthu afupi ambiri padziko lonse lapansi

15. Ku California, America kuli bulb yotchedwa Centennial yomwe inayamba kuyaka 1901 mpaka pano sinathimebe or kupsa. Ndi bulb lokhalo padziko lapansi lomwe lakhala zaka zambiri osapsa.

16. Nkhono (snail) imatha kugona kwazaka 3 osazuka inu kumati inafa koma ikugona.
17. Mkadzi wa Feoddor Vassiilyev (1707-1782) ndi mzimayi yekhayo amene anabeleka ana ambiri pakamozi (69). Ma twins ma pair 16, Ma triplets ma set 7 komanso ma set a ma Quadraplets 4. Atabeleka pompo, anamwalira...
Mwawerenga mwamaliza etii??😁😁 Sopano Pangani SHARE mma group omwe muli amzanu ena awerenge...
😊💥😁.
; Nkhaniyi yachita kumatulidwa kuchokela ku group lathu lolipilisa la Star Walero family, ndi K300/R15 pamwezi, mukationa zii pano tikumakhala kumeneku and nkhan zambiri
zikumavumbulukaso kumeneko. Tipezen ku inbox or pa Whatsapp; +265 99 000 22 70, +265 881 40 30 10 & +27 71 099 2089 k*ti mujoine lero!

06/06/2020

Kkkk

06/06/2020

My favorite is Dz

02/02/2020
26/01/2020
26/01/2020
26/01/2020
23/10/2019

HAILE SELASSIE...
(Emperor Selassie, Ras Tafari, 🦁 of Judah)
***********
Mawu oti Haile Selassie amatanthauza k*ti power of the trinity.
Haile= power
Selassie= Trinity
Power of trinity, power of unity, mphanvu za umodzi.

Haile Selassie adali mmodzi wa zidzukulu za Shewan Amhara mfumu Solomon, Sahle Selassie (Solomon mfumu yotchuka ija)
Anabadwa mu chaka cha 1892 pa mudzi wina otchedwa Erjesa Goro m'boma la Harat mu dziko la Ethiopia. Ndipo atangobadwa adapatsidwa dzina loti Lij Tafari Makonnen.
Ndipo dzinali limatanthauza k*ti mwana oopeka kapena olemekezeka.
Lij= mwana
Tafari= kuopedwa, kulemekezeka
Koma dzina loti Haile Selassie adapatsidwa nthawi yomwe amkabatizidwa.
Haile Selassie mayi ake a Woizero(Woizero ak*tanthauza mkazi)Yeshimebeti Ali Abba Jifah, ndipo mayi akewa adali mwana wa mfumu yolamula ku Wollo m'dera lina lotchedwa Dejazmach.
Bambo a mwanayu (Haile Selassie) adali a Ras Makonnen Wolde Mikael ndipo adali chidzukulu cha mfumu Sahle gavanala wa ku Harar.

Bambo akewa adali msilikali wa nkhondo ndipo adali a general ku Army, adali munthu odalirika kwambiri pa nkhondo ija ya pakati pa Ethiopia ndi Italy.
Haile Selassie adali ndik*thekera kwakukulu kokhala mfumu chifukwa choti agogo ake akazi a kuchimuna a Woizero Tenagnework Sahle Selassie, adali azakhali awo a Emperor Menelik Mfumu yachiwiri, ndiponso gogo akewa adali mwana wa Mfumu ya a Shewa(tik*ti Shewa not chewa) a Solomonic Amhala Negus Sahle Selassie. Chifukwa cha ichi Haile Selassie adali ochokera ku Makeda ndipo amkatengedwa k*ti adali mdzukulu weniweni wa Mfumu ya nzeru ya a Israel ija yotchedwa k*ti Mfumu Solomon.

Bambo ake a Haile Selassie 'am Mzungu Wakuda' a Ras Makonnen adakambirana ndi Abba Samuel Wolde Kahin k*ti azilangiza mwana wawo Haile Selassie ndi msuweni wake
Imru Haile Selassie ndi cholinga choti akule ndi makhalidwe abwino. Panthawiyi Bambo a Haile Selassie wa adali akugwirabe ntchito ngati msilikali wa nkhondo, mwatsoka mu chaka cha 1906, abambo ake adamwalira ku dera lotchedwa Kulibi, panthawiyi mk*ti Haile Selassie ali ndi zaka 14.
Next, next, mbiriyi ndi ya Haile Selassie, munthu amene ma rasta amapembedzera Mulungu kudusira mwa iye, yafupika chifukwa cha magetsi, tangokana kungokhala, komabe lawaniko kameneka, ina ibwera osadanda...
Hit more likes,comments n shares tiyambile limodzi

Timeline photos 18/10/2019

YOM KIPPUR WAR..
(Arabs reinvasion of Israel)..........
Mu chaka cha 1973 maiko a chiluya (arabs) adakhalirana pansi ndikugwirizana k*ti alande malo awo amene Israel idawalanda pa nkhondo ija idamenyedwa ya masiku 6(Mzungu Wakuda akukhulupilira k*ti adafotokonzapo kale za Israel and Six days war ndipo mwakumbukira). Maikowa adagwirizana k*ti athire nkhondo yoopsa dziko la Israel, iwowo adalimba mtima k*ti zitheka kugonjetsa dziko la Israel makamaka Chifukwa cha thandizo lochokera ku Soviet Union.
Maiko amene adakonzanso chiwembuchi adali Syria ndi Egypt ndipo Jordan
Iraq, Saudi Arabia, Libya, Tunisia, Algeria, Morocco, Cuba, Hezabolla, amkamenya nkhondoyi pothandizira Egypt ndi Syria. Maikowa amamenya nkhondoyi ndichithandizo cha ndalama chochokera ku Soviet Union. Komatu Israel idali yokha koma nayonso imkamenya nkhondoyi ndi chithandizo cha ndalama chochokera ku dziko la USA..........
Nkhondoyi idayambika mgwirizano wa Aluya utapanga attack Israel pa tsiku la Yom Kippur (ili ndi tsiku loyera la ayuda limene limakhalapo kamodzi pa chaka),ndipo mwezi umenewo udali Mwezi Oyera wa Lamadani(Muslim Holly month of Ramadan).
Patsikuli, mwanthawi imodzi
Egypt ndi Syria adadutsa ceasefire line ndipo ma Egyptians adakapanga attack Israel pa Sinai Peninsula (paja kalero malowa adali a Egypt Israel idachita kulanda pa 6days war) kumbali inayi nayonso Syria idakapanga attack ma Israelites soldiers pa Golan Heights (malowanso Israel idachita kulanda mmanja mwa Syria pa 6days War).
Patsikuli Israel idali busy kwambiri Chifukwa kwa iwowo limakhala tsiku lopaturika ndi adani awowa amkakhulupilira k*ti Kupanga attack Israel patsikuli zikhala zophweka kugonjetsa.
Kodi zidakhala bwanji?? Mzungu Wakuda akufotokoza.
Ma Egyptians adafika pa Sinai Peninsula komanso asilikali ambiri a aluya adakatseka njira pa Suez Canal.
Ena mkumafunsa k*ti kodi iwe Mzungu Wakuda Suez Canal ndichani?........
SUEZ CANAL
Suez Canal ndinjira ya madzi kapena k*ti kamtsinje komwe anthu adachita kukoza, kamtsinjeka kadarumikiza nyanja ija yofiira(red sea) ndi Mediterranean Sea kudutsira pa Isthmus (land that sticks out of the sea) ya Suez.
Kamtsinjeka kadakumbidwa mu chaka cha 1859 ndi Suez canal Company. Ndikakatali 193.3 km (120.1 miles) kalero kamtsinjeka kadali mmanja mwa Uk ndi France koma mu 1956 kadapangidwa handover mmanja mwa company ya Suez Canal Authority ya mdziko la Egypt.........
Asilikali a nkhondo okwana 800000 ndi ma tank okwana 1500 a dziko la Egypt adasonkhetsedwa, asilikali okwana 150000 ndi ma tank 1200 a dziko la Syria adasonkhetsedwanso k*ti akathire nkhondo Israel, pomwe cuba idatumiza 4000, Morocco 5500, Saudi Arabia 3000. Kuphatikiza asilikali onse ndi zida zawo 914,000–1,067,500 troops ndi
3,430–3,600 tanks
3,900–4,000 armored carriers
1,720 artillery units, 452 combat aircraft, 140 helicopters, 104 naval vessels, 150 surface-to-air missile batteries. Dziko la Israel asilikali amene adamenya nkhondoyi adali okwana 415 000 okha ndipo ma tank adali 1700......•........
Kodi zidatha bwanji? Wait for part two! (Blackouts ndi omwe achitisa k*ti nkhaniyi ifupike koma don't worry part 2 coming soon)..
Hit more likes,comments n shares mma groups! Part 2 ikufiken munthawi yake!...
...!
DJ Shuxy Phone Accessories ku Area 18A, Lilongwe. Kuchimake kwa zipangizo za ma phone za original, komanso sound system mbambande for hire. (0888795608 DJ Shuxy).
Ngati muli ndi business kapena chilichonse choti tikupangileni advertise ife a "Star Walero" ndi okomzeka k*tero, ndipo simudzakhumudwa. Tipezeni pa 0888 044 924. (Sms, Call, & Whatsapp)

Timeline photos 14/10/2019

OPARATION BWEZANI 1993.

MALAWI DEFENCE FORCE vs MALAWI YOUNG PIONEER (MYP).

^ Malawi young pioneer idapangidwa mu zaka za ma 1965 ndi malemo founding father ^Ngwazi Dr H Kamuzu Banda. Ndipo gulu ili adalipanga potengela system ya m'tsogoleli wakale wa dziko la ^Ghana Kwame Mkrumah^ cholinha chake cha movement imeneyi kunali k*ti aziphuzitsa achinyamata ntchito za umisili ndi zina zina zotero.

Mu Chaka cha 1965 padadusa chaka chimodzi chichitikileni za nkhaza zomwe boma lidapangila nduna ndi azitsogoleli ena ndi ena a mipingo omwe adathawa mudziko la Malawi Kamuzu adaganiza zolisintha gulu la ^MYP^ k*ti likhale gulu la nkhondo, ndipo ^MYP^ Kamuzu adaipezela maiko oti adzipanga sponcer mu zaka za ma 1970 ndipo maiko ena omwe amapanga suport ^MYP^ ndi a Denmark, Israel, USA, BRITAIN,TAIWAN,WEST GERMANY, maiko awa adayamba k*thandiza ^MYP^ mu zinthu za mbiri ndalama' maphuzilo' ntchito za umisili komanso zida za Nkhondo. komanso mphekesela zimaveka k*ti dziko lija la CHINA naloso limathandiza nawo gulu limeneli.

Star Walero Dzufunadzimelendevuidzidziidzi.

Kuyambila mu zaka za ma 1965 kudzafikila ma 1980' ak*ti ^MYP^ ak*ti idali ndi anthu ophuzila bwino mu dziko la ^Malawi^ komanso ena adali mu maiko akunja osachepela 10,000 School ambiri adapangidwa sponser kufikila ku university komanso ambiri mwa awa adaphuzisidwa nkhondo mwa ukadaulo.

Mu zaka za ma 1970's Dr Kamuzu Banda adapanga plan yofuna kumadziwa chili chose chomwe chikuchitika mudziko la ^Malawi^ adapanga form (SIS). SECRET INTELLIGENCE SERVICE. Yomwe anthu ake adali ochokela mu gulu limeneli la (MYP). ^SIS^ ntchito zawo zidali zofanana kwambiri ndinene k*ti kuposaso ntchito ya ^Malawi Defence force^ or kuposaso ya ^ Malawi Police^. ndipo Kamuzu adapanga zothekela k*ti boma lililose kuyambila Msanje to Chitipa # Nkhotakota to Mchinji. Pa Secondary ili yose palembedwe wa (MYP) mu ma office a (DC) Mulembedwe member wa ^MYP^ note anthu awa palibe amawadziwa k*ti ndi ma member a Malawi young Pioneer. Chifukwa nawoso akalembedwa ntchito pa School amalembedwa ngati m'phuzitsi koma eni ake amadziwa ndithu k*ti akuheilila ntchito (SIS) .

Mu zaka zimenezi za 1970's kudayamba kuonekela poyela anyamata a ^Malawi Young Pioneer^ adayamba kupasidwa mifuti ndi zina zina zohwila ntchito ngati a police komanso boma la ^Kamuzu^ lidayamba kugwilisa ntchito ma body guard ochokela ku ^Malawi Young Pioneer^ akamapita kukapangisa misonkhano komanso akamapita kwina kulikose^^ izii zidayamba kukwiyisa asilikali a Malawi Defence force komanso Malawi Police at large.

Mu zaka zimenezi akulu akulu a gulu la ^Malawi Young Pioneer^ odzieika bwino adali

^Gwanda Chakwamba
^Bakili Muluzi
^John Tembo

Pa 1 December 1993 asilikali awili aku ^Moyale Balacks ku Mzuzu adaombeledwa kuphedwa ndi Anyamata a ^MYP^ # kuuupala moto kudambwe^. anthu awa adayambana ku malo omwela mowa ku (bala) adayambana chifukwa cha hule wa ku Tanzania wa chi Swahill ndipo zotsatila zake padabuka ndewu koma a MYP nthawi imeneyo amayenda ndi futi mololedwa ndi boma pomwe asilikali samaloledwa.m'kangano uwuudayambila ku ^Town ship yotchedwa Masasa ku Mzuzu komweko. Ndipo nkhani idaveka k*ti ku Mzuzu kwaphedwa asilikali a ^Malawi^ awili ndipo amene waombela ndi Wa ^MYP^ eshiiiiiiii inu inuuuuuu ma Baracks onse kuyambila ^COBE^ KAMUZU^ BARACKS adakwiya osati masewela apatu m'k*ti mudziko la Malawi muli kale tense kamba koti idali nthawi ija anthu amayembekezela kuponya vote yoyamba, asilikali atakwiya chonchi mphekesela zidaveka k*ti akulu akulu amafuna k*ti nkhaniyi ithe mwa chisisi koma asili kali adati izi sizitha mwa chisisi iwowo abweza.

Ena mwa asili kali adanyamuka ulendo kukabweza ndewu ku MYP ndipo ndewu idayambila ku (Kamuzu Institute of youth and youth House) panopa kumatchedwa (Kamuzu Institute of Sports) yomwe panthawiyo lidali likulu la ^MYP^ Lomwe lili pafupi ndi Town Ship ya ^ Kawale mu mzinda wa Lilongwe.

Kumbukilani k*ti MYP lidali bungwe lomwe limathandizidwa ndi maiko akunja ndipo lidali ndi zida zankhondo komanso ma Interagency kuposa Malawi army olo Malawi Police, ndipo kuyambila mu zaka za ma 1970's Malawi army simasangalala ndi gulu ili monga ndafotokoza pamwambapo.

📝wa m'kulu wa asilikali wa Malawi army sadafune k*ti Malawi army ibweze olo ipange nkhondo ndi MYP mwa choncho asilikali a Malawi Army adamuika pa House arrest MAJOR Genara ^ YOHANE^ adamuzilatu juti nthawi yakwana mphavu zipite kwa anthu oyenela ndipo Malawi army idamuuza Yohane k*ti ngati iye savomeleza ma Baracjs onse athila nkhondo ma base a MYP.

1993 Malawi army top 3

^General Yohane
^General Manyozo
^Genela Liyabunya

Onsewa adali ndi m'gwilazano ku Chipani cha kamuzu mwachidule tinene k*to adaphuzila maphuzilo awo under MYP pambuyo paje anadzalowa ntchito ku Malawi army ndipo izi zidaululika mu chaka cha 1993.

Malawi army idatsekela top 3 yawo under house arrest. Ndipo idadula ma line a phone ju manyumba kwawo m'kuchosako anthu omwe amalondela ndipo lidawauzilatu k*ti mawa lake Malawi army ikulanda ma base onse a MYP (ndaiwala date) Pa radio kudalengezedwa k*ti aliyese asapite kuntchito m'mene imati 6 ocklock m'mawa Malawi army idali pali pose mu mzinda wa Blantyre. Lilongwe Mzuzu ndingoti idalanda ma Sec school ose ma office a boma ose ma admarc pomaliza ndege za helicopter zidaoneka zikuzungulila m'malele misewu ma (TATA) odzadza ndi Asilikali adatseka tseka misewu uwu udali ulendo okalanda ma base a MYP.

Part 2 comming soon.

Mu part 2 tidzanve k*ti zidatha bwanji.

Mungathe kulengeza malonda anu pa Star Walero Tipezeni pa Whatsup or call (+265 999 19 19 40).

Nkhani iyi yapangidwa Sponcer ndi (Mr Dankhuba A Nedze) from Cape Town.

Timeline photos 12/10/2019

BAFANA BAFANA 1996 CLASS
VS
MALAWI THE FLAMES

Iyi ndi team ya m'pila wa mwendo ya dziko la South Africa eni ake poichemelela amaitcha ^ Bafana Bafana^ mu zaka za 1900 team iyi imasewela nawo m'pila pa international lever koma inadzaletsedwa mu chaka cha 1957 chifukwa cha ulamulilo wa nkhaza omwe unali mu dziko la South Africa mu nthawi imeneyo ^ Apartheid^ ndipo panadusa zaka zosachepela 40 k*ti team iyi ayiloleso kusewela m'pila ndi maiko ena.

Ine ndiyambile pa ^1992^ ulamulilo wa Apartheid utaineka k*ti watsala pang'ono kuchoka pa ulamulilo bungwe loyendesa masewela a m'pila wa mwendo adalivomeleza dziko la South Africa k*ti litha kuyamba kusewela nawo pa international lever mu chaka ichi m'k*ti boma lili m'kati mokozekela kudzapanga zisankho ^ 1994^ k*ti zika ili yose ya dziko ikhale ndi mwayi osankha m'tsogoleli ambiri tikudziwa bwino k*ti apa ndi pamene ^Nelson Mandela anadzasankhidwa kukhala president wa dziko la SouthAfrica.

Masewela oyamba mu 1992 Bafana Bafana idasewela ndi team ija ya ku ^ Cameron ^ ndipo Bafana idagonja 1 kwa 0 masewela awa adachitikila pa bwalo lija lero limatchedwa ^FNB STADIUM^ nthawi imemeyo limatchedwa k*ti ^ Soccer City^

Dzufunadzimelendevuidzidziidzi

Mu chaka cha 1995 ^Bafana Bafana^ idapasidwa mwayi oti ipange host chikho chija cha ^ Africa Cup off Nation's^ izi zidachitika maiko onse a mu Africa pofuna kuonetsa chikondi ndi dziko la South Africa komanso pofuna kumusangalatsa ^Nelson Mandela^ pa ntchito yake yomwe adachitila dziko la South Africa yomenyela ufulu # politic sindilowako kwambiri lero tikambe za m'pila #

Bafana Bafana idayamba masewela ake okizekela k*ti ipange qualify monga zimachikhalila ma team akamakozekela kulimbana malo ku Africa Cup of Natsions nthawi imeneyo ma team amafunika ^ 16^ amagawidwa magulu ^4^ koma poti Bafana Bafana anali ma host anali akudziwa kale k*ti iwowo adzasewela nawo ku Ma final Stages omwe amadzachitikila mu dziko lawo la SouthAfrica. Komanso bungwe loyendesa Africa Cup off Nations lidalamula k*ti Bafana Bafana panthawiyo ikuyenela kufika mu ma quater finals posatengela kuwina olo ku gonja mu group stages.

Star Walero

Ma game Bafana onayamba kusewela ndipo inapezeka k*ti yaeinq ma game awo onse home and away ndipo idakhala top mu group lawo # take note ma team omwe amapita ku Southafrica anali ^ 16^ ndipo mu group ili lose 2 top teams limapanga qualify kupita mu ma quater finals. Koma team ija ya ^ Nigeria^ idadzabwelela itapanga kale qualify nthawi imeneyo president wa dziko la ^ Nigeria^ General SANI ABACHA^ adalamula k*ti team ya Nigeria isapite ku Southafrica. Zomwe zinaoangusa k*ti ma team apite 15 okha basi.

Bafana Bafana mu 1994 idasewela nawo ma game ofuna kupita ku Africa Cup of Nations idali froup ^5 ^ koma sidapange qualify mu 1994 Bafana idali limodzi ndi maiko aja a, Zambia, Zimbabwe,Mauritius,

1996 Malawi vs Bafana.

Venue Kamuzu Stadium ( Chichili Stadium).

Team ya Bafana Bafana idataya mbiri itawina Africa Cup of Nations pakwawo ndipo kulikose kumene imapita kukasewela imalandilidwa mwa sangala ma Stadium amadzadza sizimatengela k*ti akusewela k*ti mwa chitsazo ku Cameron, Zambia, Mauritius, Zimbabwe, Saudi Arabia, ndi maiko ena otelo zimaveka k*ti Bafana Bafana itapita kukasewela maiko amenewa ku Stadium kumafa munthu stamped polimbilana k*ti alowe mu Stadium awonele nawo team imeneyi.

Koma ine pano ndinenepo za pa Kamuzu Stadium. Tsiku linafika linali loweluka ndipo kunawala dzuwa mu m'zinda wa Blantyre, kwa nthawi yoyqmba anthu ananyamuka miyanda miyanda kuchokela ngodya zose za dziko la Malawi Chitipa, Msanje, Mchinji, Nkhotakota. Kubwela ku dzaonela m'pila pakati pa ^ Malawi the Flames vs Bafana Bafana. Nthawi m'mene imakwana 12 pm pa MBC analengeza k*ti Stadium yadzadza koma anthu omwe anali kunja kwa Stadium analiso okwanila kulowa m'kati kudzadzaso ^Kamuzu Stadium^ nthawi m'mene imakwana 1 pm ma gate anatsekedwa koma ngakhale ma gaye anatsekedwa anthu anayamba kuvutisa kufuna kulowa mu Stadium pogwesa zipata. zinthu zili chonchi nduna ya za masewela ^Dumbo Leman^ adalanfila foni kuuzidwa zoti team ya Bafana Bafana sinafike ku Stadium ndipo amaiposa kupita ku Stadium chifukwa sakanatha kudusa kukafika kuseli kwa Stadium kuja ma team amalowela ku dressing room kuchoka ku Mount Soche Hotel, apa Nduna ya za masewela idapempha Ndege ku Malawi Defence force k*ti ngati kotheka inyamule ma player a ^ Bafana Bafana^ kukawatsitsila m'kati mu Stadium apa nthawi ili 1:45 koma Game imayenela kuyamba 2:30pm. Tsiku dziko la Malawi aliyese adali ali m'mbali mwa Radio kumavesela ma update a zomwe zikuchitika ku Stadium ndipo amati akalengeza pa radio zinthu ngati iziii dziko la Malawi limaveka kugwedezeka. # 1:55 ndege ziwili za Malaei defence force zidatela pa bwalo la Kamuzu Stadium kudzasiya ma player a ^Bafana Bafana^ zitatelo m'k*ti anthu akulila ndi chimwemwe komanso kunja kwa Stadium anthu akungopondana kulimbana k*ti alowe m'kati mu Stadium nde poti Kamuzu Stadium ilibe exact figure a unduna wa Malawi Sports adalamula k*ti ma gate atsekulidwe aysesese kulowetsa anthu m'paka m'paka ena amati anthu adalowa okwanila ^90,000 M'malo mwa anthu ^35,000 that means stadium idalowesedwa over ndi anthu ^55'000^.

2:30 PM nduna ya za Masewelo olemekezeka malemo ^Dumbo Lemani^ adalankhula pa MBC radio 1 kupempha anthu ku stadium k*ti asunge bata ndi m'tendele apa m'k*ti ma team a ^Flames ndi Bafana^ atasala pabg'ono kulowa m'bwalo game idapangidwa delay ndi 15 min, mphekesela zidaveka k*ti anthu okwanila 11 adanyamulidwila ku chipatala atavulala kunja kwa stadium polimbqna k*ti alowe alowe game isanayambe.

Malawi first 11.

1.Bothwell Kuwanda

2,Meke Mwase
3,Patric Mabed
4, Lawlent Kamanga
5,Charles Manda
6,Walter Nyamilandu

7, Christopher John Banda
8,John Maduka.
9,Chancy Gondwe
10,Albert Kika M'Pinganjila
11,Ernest Chilyali Mtawali.

Bafana Bafana.

1,Andre Arendse

2,Sizwe Motaung
3,Neil Tovey,
4, Lucas Radebe
5,Willem Jackson

6,Eric Tinkler
7, Linda Buthelezi
8,, Doctor Khumalo,
9, John Moshoeu
10, Phil Masinga,
11, Shaun Bartlett

Adatulukila m'bwalo ndipo ^Steve Liwewe^ adalila mokweza pa ^MBC^ kusowa chonena kusowa cholankhula, ^ Joseph Kazembe^ naye popeleka line up m'chichewa adati zomwe amaona pa Kamuzu Stadium zidali zoti sadazionepo kuona m'mene Stadium inadzadzila, kuona team ya Bafana Bafana ikulowa m'bwalo ......

Part 2...... comming

Ngati muli ndi malonda ndipo mukufuna kulengeza pa Star Walero mungathe k*tipeza, ndife okozeka kulengeza malonda anu. Tipezeni pa #0888795608 call or whats up.

Want your business to be the top-listed Beauty Salon in Lilongwe?
Click here to claim your Sponsored Listing.

Category

Telephone

Website

Address

83 Mayani Dz
Lilongwe
MW
Other Health/Beauty in Lilongwe (show all)
Superlife Malawii Officìal Superlife Malawii Officìal
Lilongwe
Lilongwe

Superlife as a stable company aims at providing scientifically tested products to provide the wellbe

Melki Commodities Melki Commodities
Lilongwe

Securing all against food insecurity

KALVA DOR KALVA DOR
Kalva
Lilongwe, DOR

CHARĪ KAY 2008 CHARĪ KAY 2008
Zomba
Lilongwe, 2008

Malawian Charity

Dzuwa saloon and boutique Dzuwa saloon and boutique
Mchesi
Lilongwe

We sell clothes for men, women and children

Grex Starboy Kasamba Grex Starboy Kasamba
Lilongwe Street
Lilongwe

��

Naseema Tailoring & Design Center Naseema Tailoring & Design Center
Lilongwe

Ndife Akaswili posoka National wear, , School Uniform,, Za Chikwati... Soccer Jersey ndi Za azibambo.... Tipezeni sitidzakukhumudwitsani

Hyprand the goat Hyprand the goat
Chisapo
Lilongwe

This paga ndiyam boro odziw kuntchena

Kisha beauty spot Kisha beauty spot
Lilongwe
Lilongwe

STC 30 STC 30
Lilongwe

Superlife STC30 is the origin of stem cell therapy in the treatment of human ailments!!!