Chakhaza - A - ECD & CBCC Social Network.
Ili ndi gulu lomwe limayang,anila sukulu za mmela mpoyamba kwa TA chakhaza ku Dowa. Gululi limayang,
👆👆Ndi njira zomwe timasewelela ndi Ana(kuwaphuzitsa) kuti athe kudziwa zinthu zosiyana siyana.
Zipangizo zimenezi ndi zodzikonzela zomwe Alezi amatha kukonza zomwe zimapatsa chidwi ana pa Maphunziro.
Ndife akadaulo posula Alezi(aphuzitsi) a Mmela mpoyamba ngati kwanuko mulinazo sukulu za Mmela mpoyamba ka ndi za Boma kapena za Privet ndipo mukufuna asulidwe sivuto magawo onse 8 a kaphuzitsidwe ka mwana komaso magawo 6 a kakulidwe ka mwana timazitha
TIPEZENI ku lnbox or imbani foni yomwe ili pa tsamba lathuli
MMELA MPOYAMBA 🔥🔥🔥🔥🔥🔥
CHAKHAZA A ECD EDUCATION NETWORK.
Uwu ndi nkumano Wa
Mafumu
Alezi
Acommettee
Alangizi a CPW.
Omwe wachitika Loweluka pa 16 December 2023 pa cbcc ya Nakutepa,, Gvh Nakutepa,, Senior Chief Chakhaza ku Dowa.
MFUNDO ZIKULU ZIKULU ZA MSONKHANO
🌹Kulimbikitsa ubale pakati pa Alezi ,, Akomit ndi Mafumu
🌹 Kulimbikitsa Ana komaso makolo kupita ndi kukayamba sukulu za Mmela mpoyamba.
Kugawana nzeru momwe angapangile chitukuko cha Block ndi Zina
Sukulu za Mmela mpoyamba zikulimbikitsa kusula Ana kuti akhale anzeru.
Chakhaza ECD 🔥🔥🔥🔥🔥🔥🔥🔥
🛑 KUYANKHA MAFUSO A KU INBOX KOMASO PA COMMENT BOX 🛑
1️⃣Ndi chifukwa chiyani Alezi salandila kangachepe
Fuso ili lachokela Kwa a Laston Naphata.
✍️Boma likadali nkati kupanga kupanga ndondomeko ya momwe ingamapelekeke kangachepe Kwa Alezi amenewa chifukwa cha kuchuluka Kwa Alezi omwe alipo okwana 36000 Malawi yonse.
Koma Alezi ena omwe amayang, anila Alezi anzawo(MENTORS) Anayamba kulandila Kangachepe.
2️⃣NDI CHIFUKWA CHIYANI OPHUZITSA NURSERY SCHOOL AMATCHEDWA ALEZI MMALO MOMATCHEDWA APHUZITSI CHIFUKWA AMAPHUZITSA ANA ❓
Fuso ili lachokela Kwa a Henry Chisoso
✍️Ku nusery school kulibe mphuzitsi chifukwa Ana akumeneku saphuzila monga amachitila ku primary ayi koma amadziwa zinthu kudzela mu nkusewela komaso Iwowa ndi Anthu omwe amachita kudzipeleka kuti amasewela ndi Ana moleza mtima posayang, ana nkhope kapena kukondela ndiye amayenela kukhala Oleza mtima ndichifukwa amatchedwa Alezi.
3️⃣KODI OMWE AMAPHUNZITSA NUSERY SCHOOL KOLEJI YAKE AMAKAPANGILA KUTI ❓
Fuso ili lachoka Kwa Peter Singini
✍️Ophuzitsa ana ku Mmela mpoyamba sapita ku college monga amachitila ku primary ayi koma amachita maphunziro awo a sabata ziwili 14 days komwe amakaphunzira momwe angasulire ana kudzela mu nkusewela.
4️⃣KODI OPHUZITSA KU MMELA MPOYAMBA AMASANKHIDWA MOTANI ❓
Fuso ili lachoka Kwa a Memory Banda
✍️Amasankhidwa kudzela ku Mafumu koma omwe angakwanitse komaso Odzipeleka ndi omwe anapitako ku school koma Ali nzika osati oyendayenda.
5️⃣KODI ZOMWE APHUZITSI A SUKULU MMELA MPOYAMBA AMAPHUZITSA AMAZITENGA KUTI ❓
Fuso ili lachoka Kwa a Chrisy Yasini
✍️Zomwe amasulila Ana Alezi amazitenga mu syllabus yomwe ili ndi formula ya kaseweledwe ka Ana komwe Kali ndi magulu 8 a zoseweletsa ana komaso magulu 6 a kakulidwe ka Ana.
🌹🌹➡️ CHIDZIWITSO ◀️🌹🌹
Sukulu za ku Mmela mpoyamba,,, nusery school saphuzitsa ngati ku primary ayi koma kusula Ana kudzela mu nkusewela nawo.
Mwana amaloweza zinthu kwambili kudzela mu
Nyimbo
Masewelo
ZIKOMO CHIFUKWA CHA MAFUSO ANU
🙏🙏🙏🙏🙏🙏🙏🙏🙏
Uwu ndi nkumano Wa Alezi omwe umachitika pa mwezi Cluster Meeting pomwe Alezi amakambilana ndi ku gawana zomwe zinachitika mkati mwa mwezi.
Dowa District,, TA Chakhaza posatengela kuti Alezi amagwila ntchito modzipeleka koma popanda MALIPILO posula ana pa Maphunziro,, Alezi amakumana pamodzi ndi a
➡️Alangizi
➡️Monsters
➡️ Cluster Excective commettee
➡️ECD EDUCATION NETWORK
Pofuna Kulimbikitsana kuti ana akhale ndi nzeru komaso opanda mantha pomwe akukayamba ku primary.
Pamene Boma likulimbikitsa ana kupita ku school,, ku School za Mmela mpoyamba kulimadandaulo ochuluka monga
Kusowa Kwa maphunziro a Alezi
Kusowa Kwa maphunziro ya a Commettee momwe angangwilile ntchito zawo
Kusowa support ya Mafumu komaso community.
Umu ndi mmene zinalili lolemba pa 4 December 2023 pomwe Alezi amalandila ma Register kamaso ku phuzitsidwa momwe angalembele ma record ya Ana a Mmela mpoyamba,, Nursery school kamaso kusungila .
Izi zinachitika pa cbcc ya Mponela TA Chakhaza ku Dowa ndipo amagawa katunduyu ndi a Langizi a CPW Mr Pililani Siliya ndi Kondwani Chasowa
Sukulu za Mmela mpoyamba ndi mbambande ndipo yemwe satumiza mwana wake ku sukulu za Mmela mpoyamba saganiza bwino chifukwa ndiyo Foundation ya maphunziro ya mwana.
CHAKHAZA ECD EDUCATION NETWORK ndi akadaulo pa nkhani yosula Alezi momwe angasewelele ndi Ana komaso kuwateteza pa magulu 8 osewelera ndi Ana komaso magulu 6 a kakulidwe ka mwana.
Msonkhano wa pachaka Wa pakati pa Mafumu,, Acommettee,, Alesi ndi Social Education Network.
Msonkhano uwu unali pa Mtsukamakoza Zone
Cholinga cha msonkhano
Kudziwa momwe chitukuko chikuyendela ku ma Nursery school komaso mgwilizano ukuyenda bwanji.
Cholinga ndi kufuna Kutukula maphunziro ya Ana pa Maphunziro.
MALINO CBCC TA CHAKHAZA ku DOWA.
🌼Ana kuongola minyewa ikulu ikulu ndi ing, ono ing, ono.
Umu ndi mmene sukulu za Mmela mpoyamba zikuchitila Kwa Senior Chief Chakhaza ku Dowa kusula Ana kuti akhale anzeru pomwe akukayamba Standard 1 ku primary.
Anawa kuti azikula athanzi komaso kukhala a Mphamvu,, Bungwe la
🌹FEED THE CHILDREN m, bomali likupeleka Ufa ku ma cbcc kuti ana azikula mwa thazi asamanyentchele mu program yotchedwa
✍️AKULE NDI THANZI.
Program imeneyi yathandizila ana a ku sukulu za Mmela mpoyamba kumachita bwino pa maphunziro awo komaso Kukula mwa THANZI pa Umoyo wawo.
Monga mukuona chithuzi chinacho ana AKUDYA phala pomwe Ali nkati mwa maphunziro awo.
CHAKHAZA ECD SOCIAL EDUCATION NETWORK ikuchitila umboni momwe Ana akukulila ndi kukhala athazi pa Umoyo wawo komaso Nkalasi pomwe akulandila VITAMIEL kuchokela ku FEED THE CHILDREN.
Anawa akakhuta ndipamene amakwanitsa kupitiliza maphunziro awo pa magawo 8 osewelera ndi Ana komaso magulu 6 a kakulidwe ka Ana
CHAKHA A ECD Education Network imathavkuphuzitsa zonsezi kusula Alezi kuti asamasowe poyambila kuphunzitsa Ana.
TIPEZEN KU INBOX
CHAKHAZA ECD SOCIAL EDUCATION NETWORK.
Uwu ndi nsonkhano Wa pa Chaka omwe unachitika pa center ya ZINAN, DALA ku zone ya CHIFUKULA.
Chakhaza A ili ndi ma cbcc 87 ma zone 5.
Nsonkhanowu panali
🌹 Mlangizi Wa social (CPW)
🌹GVH ZINADALA
🌹Mafumu
🌹 Acommettee
🌹Alezi
🌹 ECD Education Network
🌹Mentor
🌹F, F. Field Faciliteter.
Zomwe zinamanga nthenje
🪴Chitukuko cha pa cbcc
🪴 Mgwilizano Wa a Mafumu,, commettee,, Alezi,, Ana komaso makolo
🪴 Kulimbikitsa kukhala ndi madimba,, Bank nkhonde komaso Munda olimapo mbewu.
Pempho linakula pa nsonkhanowu ndi pempho la Alezi ndi a commettee chifukwa chosasulidwa momwe angathe kusamalila Ana komaso momwe angawa phunzitsile(kusewela ndi Ana momwe angayendetsele chitukuko.
ECD EDUCATION NETWORK CHAKHAZA A itha kukwanitsa kusula Alezi ndi a commettee momwe angangwilile ntchito bola Bungwe Lina litathandizapo kumbali ya Ndalama.
Chakhaza A. Kuli mabungwe omwe akuthandiza kumbali ya Nursery school monga
🌻 World vision
🌻 World Bank
🌻Feed the children
Monga maphunziro ya Alezi,, Kumanga ma Block azitsanzo komaso kugawa Ufa ku Ana a pa Cbcc.
CHAKHAZA ECD SOCIAL EDUCATION NETWORK ndi. 🔥🔥🔥🔥🙏🙏🙏
MALINO CBCC ka Senior Chief Chakhaza ku Dowa,, Gvh Chinguwo.
Iyi inali morning circle pomwe Mulezi amakonzekeletsa ana pa maphunziro apa tsikuro la 20 NOVEMBER 2023.
Ana akuongola minyewa ikulu ikulu ndi ing, ono ing, ono.
Ku Mmela mpoyamba ana amasewela( kuphunzila) mmagawo or magulu 8 ndi magawo 6 a kakulidwe ka mwana
Mwana oyambila ku Mmela mpoyamba amakhala ndi nzeru ku primary.
Mwana amaphunzira kudzela mu nkusewela
Ndife akadaulo posula Alezi(aphuzitsi)a Mmela mpoyamba
ECD EDUCATION NETWORK.
CHAKHAZA A M, BOMA LA DOWA
✍️Uwu ndi nsonkhano Wa pa Chaka omwe wachitika pa 18 November 2023 pa cbcc ya Kapondo Senior Chief Chakhaza ku Dowa.
✍️Chakhaza A ili ndi ma cbcc 87 omwe adagawidwa mma center 5.
Msonkhano uwu wachitika ku center ya Chinkhwili ndi ma cbcc 17.
MFUNDO ZA MSONKHANO.
✍️🧎Kodi mchakachi chitukuko komaso mgwilizano Wa pakati pa
🪴Mafumu
🪴Acommettee
🪴Alezi
🪴Makolo
🪴Ana
Ukuyenda bwanji ❓
🛑 CHAKHAZA ECD EDUCATION NETWORK ITHA KUKWANITSA KUSULA ALEZI KOMASO A KOMITI NDIPO NDI AKADAULO NDIPO BUNGWE LOMWE LIKUFUNA KUPANGITSA CHISULO GULULI LIMATHA.
NGATI PALI MA PRIVET NURSERY SCHOOL NDIPO MUKUFUNA ALEZI ANU ADZIWE MOMWE ANGASULILE ANA TIPEZENI KU INBOX TIMVANE.
MWANA OYAMBILA KU MMELA MPOYAMBA AMAKHALA NDI NZERU KU PRIMARY.
Bungwe la World Bank M, Boma la Dowa Kwa Senior Chief Chakhaza lolemba pa 9 November 2023 linali ndi zokambila ndi Mulangi komaso ECD,, Education Network.
Malingana ndi mulangizi Wa Bungweli yemwe akuyang, anila kudelali a Crara kelele ,, amafotokoza momwe Bungwe la World Bank yagwilila ntchito mzaka zawo.
Bungweli limathandiza Sukulu za Mmela mpoyamba monga
Maphunziro ya Alezi
Maphunziro ya a Commettee
Kumanga ma Block ya ma cbcc achitsanzo.
Kuphuzitsa kulima madimba
Kupeleka mbuzi ku ma Model
Mulangizi Wa Bungweli anakumana ndi magulu awili pa nkumanowu monga
ECD Education Network Chakhaza A
ECD Education Network Chakhaza B
Ma guluwa athokoza World Bank kudzela mwa mulangizi Crara Kelele pa nchito yomwe Bungweli likuchitha kuthandiza sukulu za Mmela mpoyamba ku Malawi.
Bungwe la World vision, Kasangadzi AP ku Dowa la chisanu pa 17 November 2023 agawa katundu othandizila Kutukula miyoyo ya Ana pa Maphunziro ya Mmela mpoyamba.
World vision imathandiza ku Mmela mpoyamba pa zinthu izi
Maphunziro ya a Lezi
Maphunziro ya a commettee
Zipangizo zophuzitsila
Kumanga ma Block ya Ana ndi Zina
Sukulu zambili zomwe zalandila katunduyu zayamikila kwambili kuti tsopano madzi akhala osamalika.
🗣️AKATSWILI PA NKHANI ZA MAPHUNZIRO KUKAMBILANA ZA KAKULIDWE KA ANA KU MMELA MPOYAMBA
Choyamba tidziwe mau akuti
👉CBCC👈
Mauwa amatanthauza kuti,,
✍️ C,,, Community
✍️B,,, Basic
✍️C,,, Children
✍️C,,, Care
Mwachidule
Malo a chisamaliro cha Ana(Mmela mpoyamba).
🗣️Malowa amayang, ana kakulidwe ka mwana.
Pamene Boma linatsindika kuti mwana oyambila ku phunzitsa ku sukulu za Mmela mpoyamba amakhala Wa nzeru komaso ochangamuka.
Choncho Boma lidayang, ana ndi kutsindika pa kaphuzilidwe // kaseweledwe ka anawa pa magawo awa,,
🩸Kukula mu Uzimu
🩸Kukula mu chikhalidwe
🩸Kukula mu nzeru
🩸Kukula mu chilankhilo
🩸Kukula mu umunthu
🩸Kukula mu mu chiphunzitso
🗣️Njila 6 izi ndi zomwe zimapangitsa kuti mwana akule ndi kukhala Wa nzeru ku sukulu ndipo akaphonya izi AMASOKONEKELA
🗣️Ndi sukulu za Boma za Cbcc zomwe a Lezi //Aphunzitsi ake amatsayila izi.
Mwana akabadwa amaysmba ndi Nkaka Wa mmawere
Kenaka phala la madzi
Kenako lolomba + Nsima + zakudya Zina mwa ndondomeko mpakana minyezi 6
Ndiye mwana kungobadwa ndi kumuyambitsa Nsima mwamupweteka ameneyo,, sukulu Zina za Cbcc Maka za ma Private za anthu ana a Cbcc amawaphunzitsa mmalo mosewela nawo
🤦👉IFE NDI AKADAULO PA ZA MMELA MPOYAMBA NDIPO TITHA KUKUSULILANI AZIPHUZITSI ANU///ALEZI ANU KUTI ADZIWE KUTAKAZA UBONGO WA MWANA.
PANGANI 👉 LIKE PAGE INO NDI KUPANGA SHERE KWA ANZIZANU KUTI ADZIWE NAWO
❤️❤️❤️❤️❤️❤️❤️❤️❤️❤️❤️❤️❤️❤️❤️❤️
🤔DZIWANI ZA SUKULU ZA MMELA MPOYAMBA(NURSERY SCHOOL)
➡️ Nursery school ndi chani ❓
🤝 Nursery school ndi maphunziro ya Ana omwe asanathe zaka 5 omwe amaphunzira pamodzi kudzela mu kusewela powakonzekeletsa kukayamba Std 1 ku primary school.
➡️Mitundu ya Nursery school
Sukulu zimenezi ndi Mtundu ndi umodzi koma zimachitika mmagawo awili
Ana zaka ziwili komaso zitatu
Ana a zaka zinayi komaso zisanu
Apa ma Gulu awiliwa amaphunzira Malo osiyana chifukwa ena ndi ozindikila ena ayi
Sukuluzi zimapangidwa mmagulu angapo monga
Sukulu za Boma
Sukulu za mipingo
Sukulu za privet
⚠️ CHOLINGA CHA NURSERY SCHOOL ⚠️
🚦Kuti ana aphunzire kukhala pa Gulu.
🚦Kuti ana adziwe zinthu Ali Ang,ono
🚦Kulera,, kusamala Ana
🚦Kuwakonzekeletsa chiyambi cha maphunziro
⚠️🩸KAPHUZITSIDWE KA SUKULU ZA MMELA MPOYAMBA 🩸⚠️
Sukulu izi zimakhala ndi Alezi,, osati mphuzitsi.
🦜Mulezi ndi Munthu yemwe amasamala ndi kusewela ndi Ana.(phada,,Jingo).
🦜 Mphuzitsi ndi Munthu yemwe amaphunzitsa Ana. (EG,, kuwonkhetsa,, kiwelenga).
⚠️NOTE⚠️
Ndondomeko ya Boma ndiyoti Ana a Nursery school azidziwa zinthu kudzela mu kusewela pa magulu 8 osewelera ndi Ana.
Sukuluzi sitiphuzitsa chifukwa Ana amakhala achichepele koma kusewelanawo.
Mukadzaona sukulu za Nursery ena akuphuzitsa ndiye kuti ndi primary imeneyo
Ku nursery school kulibe 2+3 kapena lembani mau oti____❓
Koma kuli tiyeni tijowe ulendo 5 kapena 👉uwo ndi Mtengo.
Kawili kawili sukulu za privet ndizo zimaphunzitsa ku Nursery//Mmela mpoyamba kufuna kukopa anthu kuti makolo azipeleka ndalama zambili komwe kuli kuononga ubongo Wa mwana
Mwana amayenela azidziwa zinthu pang, ono pang, ono kuti ubongo wawo usasafale.
Mwana amadziwa zinthu kudzela mu kusewela ndipo saiwala konse.
Block ya Ana a mmela mpoyamba imafunika kuti ikhale ya zipinda zitatu
Malo opumila
Malo ophunzililapo ana a zaka ziwili mpaka zitatu
Malo ophunzililapo ana a zaka zinayi mpakana zisanu.
🛑 FORMAT YA MMELA MPOYAMBA🛑
👆👆Tidzapitiliza mtsogolomu
Like our page
Awa ndi Ana apa sukulu ya Mponela 2 Cbcc Kwa TA Chakhaza ku Dowa
Tsiku limeneli mlezi amasewela // Ku phunzitsa ana pa magawo 6 a kakulidwe ka mwana ndipo anatenga Gawo la kakulidwe ka mwana mu Uzimu
Gulu lino ndi akadaulo kusula aphuzitsi a Nursery school kuti ana phuzile bwino komaso alezi//Aphuzitsi akhale ndi Luso
Ofuna kudziwa zambili za momwe Nursery school lmayendrle tipezeni ku lnbox yathu kapena lmbani fon pa number yomwe muyipeze pa page yathu lno.
Makolo ochuluka tsopano ayamba kuzindikila ubwino a school za Mmela mpoyamba,, Nursery school.
Mwana kuti aphunzile bwino akuyenela kuyamba ku school za Mmela mpoyamba.
Mwana akafika zaka ziwili mutumizeni kuti akaphunzire chikhalidwe ndi kuongola minyewa yaikulu ndi yaing, ono
Ife ndi akadaulo osula ana a mmela mpoyamba.
Mulibwanji. Tinati ziii ma update chifukwa Cha mavuto ena koma tsopano tayambapo
👉Ulezi wabeba. Kodi mukudziwa kuti Alezi ena adayamba kulandila ndalama? Mentors.
Group ino ILISO pa WhatsApp ofuna kujoina abwele Ku inbox ataika number yake
Mulibwanji
Tsopano tiyambaso kukupatsilani ma update ya Mmela mpoyamba,, Nusury school
Ngati lnuyo ndi mulezi//Caregiver kapena m,bale wanu,, tili ndi group pa WhatsApp la Nursery school// Mmela mpoyamba kapena kuti ECD.
👉Ofuna Ku joina andipange Hy ndi kulemba mau oti,,
Mmela mpoyamba
ECD ndi kutumiza pa number
👉 0999344584 ndipo apangidwa add pa group la pa WhatsApp limeneli.
Muzimva ndi kuona momwe anzanu skusewelela komaso kuphunzitsa Ana.
Mulibwanji
Kodi mwawakonzekeletsa Ana zaka 5 omwe akukayamba Std 1_ Ku ma primary??..
Mulezi komaso sukulu ya moyo lmadziwika ndi zipatso zake ndiko kutumiza Ana Ku primary.
Dziwani izi.
👉 Sukulu za Mmela mpoyamba ntchito yake ndi kusewela ndi Anaonga malamuro a boma ndi ndondomeko zake zidakonzedwela.
👉 Alezi omwe anasulidwa ndi mabungwe ena mothandizana ndi Boma akudziwa izi.
👉 Kawili kawili pamakhala kusiyana pakati pa sukulu za Boma ndi za private chifukwa a private amaphuzitsa ngati Ku primary pamene a Boma ama sewela ndi ana potsata magawo eight (8) ophuzitsila.
👉 Mwana amafunika kumukonzekeletsa asanadziwe zazikulu.
Mulimbwanji?.
Chifukwa cha nyengo inasimtha kakulidwe ka Anthu. Ndiye mwana akakwanitsa chaka kapena zaka ziwili akuyenela kukayamba sukulu za mmela mpoyamba(nursary schooi.) Kuti adzakhale wachidwi pa maphunziro.
👉 Tisaiwale mwana akakwanitsa Minyezi 6 ayenela kudya zakudya za magulu 6 kuti akule mwa thanzi komaso adzakhale wa nzeru pa maphunziro ake,, osaiwala kuti akadwala thamangilani kuchipatala
Mulibwanji.
Konzekelani zotsekulila ma kalasi week ikubwelayi.
Mulezi ayenela kutsata ndi kudziwa izi
📢 Kudziwa Ana omwe akuphunzitsa
📢 Kudziwa vuto la mwana
📢 Kudziwa chikhalidwe ndi mtundu wa mwana
📢 Kudziwa chikhalidwe cha Makolo
🔊 Mulezi akuyenela kudziwanso izi
🔰 Magulu osewelela ndi Ana monga
🔋 ZOIMBA IMBA
🔋 ZA LUSO
🔋 ZOMANGA MANGA
🔋 ZOGWILA GWILA
🔋MASEWERO APANJA
🔋 ZA CHILENGEDWE
🔋 ZOWELENGA WELENGA
Awa ndi ma gulu 8 ophunzitsila
📢 Mlezi azidziwaso ma gulu 6 a kakulidwe kamwana,, mwa chitsanzo
🔰 Kukula munzeru
🔰 Kukula M chikhalidwe
🔰 Kukula mu Uzimu ndi zina
📢 Pa nthawi imeneyi mulezi akuyenela kukonzekeletsa Ana omwe akukayamba STD 1 mu September uno.
👉 Ana onse a zaka 5 Ku nursury akuyenela kumakapitako Ku primary kukaona momwe Ana anzawo akuchitila kukana kukaona chilendo.
📢 Mulezi azikhala oleza mtima ndi okonda mwana aliyese.
🙋 Page ino iliso pa WhatsApp ndipo ofuna Ku joina angolemba bau oti ECD ndi kutumiza pa nber 👉 0999344584 mupangidwa add
Kumbukulani kuti page ino iliso pa WhatsApp ndipo ofuna Ku joina alembe massage yoti Chakhaza ndi kutumiza pa 0999344584 ndipo mupangidwa add
ALEZI,, Aphunzitsi a sukulu za Nkomba mphala tsopano sangalalani nda mukulembedwa ntchito m,boma